Ezekiel 20:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma ana ao nawonso adandipandukira. Sadatsate malangizo anga, sadamvere malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Ndiponso adaipitsa masiku anga a Sabata. Tsono ndidaganiza zoŵalanga mokwiya ndi kuŵalipsira m'chipululu momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anawo anapandukira Ine, sanayenda m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwacita, amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'cipululu.