Ezekiel 20:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵalekerera kuti adziipitse ndi zopereka zao, makamaka pakupereka ana ao achisamba ngati nsembe zootcha. Ndidatero kuti ndiŵadetse nkhaŵa, ndipo kuti adziŵe kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.