Ezekiel 20:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, lankhula nawo tsono Aisraele, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Makolo anu adandinyozanso poleka kundikhulupirira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa icinso atate anu anandicitira mwano pakundilakwira Ine.