Ezekiel 20:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamene ndidaŵaloŵetsa m'dziko limene ndidaachita kulumbira kuti ndidzaŵapatsa. Kulikonse kumene adaona chitunda chachitali ndi mtengo wogudira, kumeneko ankapereka nsembe ndi zopereka zao zondikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma, ndiponso nsembe zazakumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya citunda ciri conse cacitali, ndi mtengo uli wonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, napetekapo nsembe zao zondiputa, aponso anacita pfungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.