Ezekiel 20:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono uŵauze Aisraele kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi mudzadziipitsa monga momwe makolo anu adachitira ndi kusokera popembedza milungu yao yonyansa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anachitira makolo anu? Muchita chigololo kodi kutsata zonyansa zao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anacitira makolo anu? mucita cigololo kodi kutsata zonyansa zao?