Ezekiel 20:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, ndidzakulamulani ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga ndili wokwiya kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.