Ezekiel 20:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakuchotserani anthu amene amandipandukira ndi kundichimwira. Ndidzaŵatulutsa m'dziko limene akukhalamolo, koma sadzapondamo m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawaturutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israyeli; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.