Ezekiel 20:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu nomwe ndidzakulandirani ngati nsembe za fungo lokoma, nditakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina, ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikira. Pamenepo ndidzaonetsa ungwiro wanga pakati pa inu, ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati pfungo lokoma ndidzakulandirani pakukuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukucotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.