Ezekiel 20:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono inu a m'banja la Israele mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzakuchitirani zabwino, osakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zopotoka, kuti choncho dzina langa lilemekezeke. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditacita nanu cifukwa ca dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa macitidwe anu obvunda, nyumba ya Israyeli inu, ati Ambuye Yehova.