Ezekiel 20:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uliwuze kuti, Chauta akuti mumvere mau ake, Iye akunena kuti, ‘Ndidzakuyatsa moto, ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse youma ndi yaiŵisi yomwe. Malaŵi ake adzakhala osazimika, ndipo aliyense kuchokera kumwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uli wonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uli wonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.