Ezekiel 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake uŵauze mau anga akuti, Pa tsiku limene ndidasankhula Israele, ndidalumbira kwa zidzukulu za Yakobe, ndipo ndidadziwulula kwa iwo ku Ejipito. Ndidalumbira ndi kuŵauza kuti, ‘Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israele, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Ejipito, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israyeli, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Aigupto, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;