Ezekiel 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo ndidalumbira kwa iwo kuti ndidzaŵatulutsa m'dziko la Ejipito, kupita nawo ku dziko limene ndidaŵapatsa, dziko lamwanaalirenji, lokongola kwambiri kupambana maiko ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwaturutsa m'dziko la Aigupto, kumka nao ku dziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;