Ezekiel 20:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinanena nao, Ali yense ataye zonyansa za pamaso pace, nimusadzidetsa ndi mafano a Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.