Ezekiel 20:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma adandipandukira, adakana kundimvera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adasiya zonyansa zake zimene ankasangalala nazo. Palibe amene adasiya mafano a ku Ejipito. Tsono ndidaganiza zoŵaonetsa ukali ndi mkwiyo wanga ku Ejipito komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataya yense zonyansa pamaso pace, sanaleka mafano a Aigupto; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Aigupto.