Ezekiel 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma sindidachite zimenezo, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene Aisraele ankakhala nawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo pakutulutsa Aisraele m'dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto.