Ezekiel 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulire ndipo ufuule, iwe mwana wa munthu, chifukwa zonsezi zidzagwera anthu anga. Zidzagweranso akalonga a Aisraele. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Nchifukwa chake udzigunde pa chifuŵa mwachisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu, pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga; zidzagweranso akalonga onse a Israeli. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pfuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israyeli, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; cifukwa cace panda pancafu pako.