Ezekiel 21:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma iwe mwana wa munthu, losa, ndipo uwombe m'manja. Lupangalo lidzagwe kaŵiri ngakhale katatu, ndiye kuti lupanga lophera. Ndilodi lupanga loononga anthu koopsa, limene likuŵazungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitilize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuluyo, limene liwazinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono mwana wa munthu, nenera ndipo uwombe mʼmanja. Lupanga likanthe kawiri ngakhale katatu. Limenelo ndilo lupanga lophera anthu. Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa limene likuwazungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitirize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuruyo, limene liwazinga.