Ezekiel 21:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga adzataya mtima, ndipo ambiri adzagwa. Ndaŵaikira lupanga laphuliphuli. Ha, lupanga lidapangidwadi kuti lizing'anipa ngati mphezi, ndipo azilisolola nkuphera anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndawayikira pa zipata zawo zonse lupanga laphuliphuli kuti ataye mtima ndiponso kuti anthu ambiri agwe. Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndalozetsa nsonga ya lupanga ku zipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kucuruke; ha! analituula linyezimire, analisongoza liphe,