Ezekiel 21:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro pa miseu iŵiri imene mfumu ya ku Babiloni ingathe kudzeramo, pobwera ndi lupanga. Iŵiri yonseyo idzakhala yochokera ku dziko limodzi. Uike chikwangwani pa mphambano ya miseu yopita ku mzinda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babiloni; zonse ziwiri zichokere dziko lomwelo; nulembe chizindikiro cholozera, uchilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babulo; zonse ziwiri zicokere dziko lomwelo; nulembe cizindikilo colozera, ucilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.