Ezekiel 21:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mfumu ya ku Babulo aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mibvi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi ciwindi.