Ezekiel 21:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'dzanja lake lamanja muli muvi wa ula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumu iyenera kukalalika za kupha anthu ndiponso kufuula mfuu wankhondo. Iyenera kupanga makina othyolera zipata, kuunda mitumbira yankhondo ndi kumanga nsanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'dzanja lake lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kufuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'dzanja lace lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kupfuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.