Ezekiel 21:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Mwandikumbutsa zolakwa zanu, ndipo kundiwukira kwanu kwaonekera poyera. Mukuwonetsa machimo anu pa zochita zanu zonse. Nchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu povumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti machimo anu aoneka m'zonse muzichita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu pobvumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti macimo anu aoneka m'zonse muzicita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.