Ezekiel 21:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono iwe mwana wa munthu, ulalike kuti, ponena za Aamoni ndi manyozo ao, Ine Chauta ndikuti, “ ‘Lupanga, lupanga alisolola kuti liwononge. Alipukuta kuti liwononge, kuti ling'anipe ngati mphezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti, “ ‘Lupanga, lupanga, alisolola kuti liphe anthu, alipukuta kuti liwononge ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za citonzo cao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.