Ezekiel 21:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uliwuze dziko la Israelelo kuti Chauta akuti, ‘Ndimati ndilimbane nawe. Choncho ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndiphe anthu ako, abwino ndi oipa omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuziti kwa dziko la Israyeli, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'cimace, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.