Ezekiel 21:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu m'dziko mwanu momwe. Palibe amene adzakukumbukiraninso. Ndatero Ine Chauta.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe. Simudzakumbukiridwanso pakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndacinena.