Ezekiel 21:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akakufunsa chifukwa chake chimene ukubuulira, uŵayankhe kuti, ‘Ndikubuula chifukwa cha nkhani zimene ndamvazi. Zikadzachitika zimenezo, mitima idzangoti fumu, ndipo manja ao onse adzalefuka, mpweya wao wonse udzaŵathera, onse m'maondo mwao mudzangoti zii. Zikubwera, zidzachitikadi!’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo cifukwa ninji? uzikati, Cifukwa ca mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uli wonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uli wonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona irinkudza, inde idzacitika, ati Ambuye Yehova.