Ezekiel 22:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena amachita chigololo ndi akazi a anzao, ena amachita zoipa ndi apongozi ao. Enanso amaipitsa alongo ao, ana a atate ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena amachita chigololo ndi akazi a anzawo, ndipo ena, mopanda manyazi, amayipitsa mkazi wa mwana wawo. Palinso ena amene amayipitsa alongo awo, ana aakazi a abambo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina anacita conyansa ndi mkazi wa mnansi wace, winanso wadetsa mpongozi wace mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wace mwana wamkazi wa atate wace.