Ezekiel 22:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga muja anthu amasonkhanitsira siliva, mkuŵa, chitsulo, mtovu ndiponso chitini m'ng'anjo, nasonkheza moto kuti uzisungunule, ndimo m'menenso Ine ndidzakusonkhanitsireni ndili wokwiya ndi waukali. Ndidzakuikani m'kati mwa mzinda ndipo ndidzakusungunulirani m'menemo ngati m'ng'anjo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga asonkhanitsa mtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi ntovu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzivukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo, mtovu ndi chitini mʼngʼanjo ndi kusonkhetsa moto kuti azisungunule, motero Inenso ndidzakusonkhanitsani ndili wokwiya ndi waukali, ndipo ndidzakuyikani mʼkati mwa mzinda, ndikukusungunurani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga asonkhanitsamtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi ntobvu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzibvukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.