Ezekiel 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ake ali ngati mikango yobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengo wapatali. Akazi ambiri aŵasandutsa amasiye mumzindamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ake mu mzindamo ali ngati mkango wobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengowapatali, ndiponso asandutsa amayi ambiri kukhala amasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali ciwembu ca aneneri ace pakati pace, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda cuma ndi za mtengo wace, acurukitsa amasiye pakati pace.