Ezekiel 22:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe ake omwe aphwanya malamulo anga, ndipo aipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Sadaphunzitse anthu kusiyana kwake pakati pa zoyenera pa chipembedzo ndi zosayenera. Sasamala masiku anga a Sabata, motero anthu sandilemekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe ake amaphwanya lamulo langa ndi kuyipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Saphunzitsa anthu kusiyana kwa zinthu zoyenera pa chipembedzo ndi zinthu zosayenera. Sasamalira za kusunga masabata anga. Motero Ine ndimanyozedwa pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ansembe ace acitira coipa cilamulo canga, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zosapatulika, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.