Ezekiel 22:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo aneneri ake abisa zimenezi monga muja amachitira anthu popaka njereza, amaziphimba ndi zimene amaona m'maloto ao abodza ndi m'maula ao onama. Amati, ‘Ambuye Chauta akunena zakutizakuti,’ pamene Ine Chauta sindidalankhule konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pace, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova posanena Yehova.