Ezekiel 22:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu am'dzikomo amasautsa anzao ndiponso amaba. Amazunza osoŵa ndi osauka. Amavutitsa alendo posaŵachitira zinthu mwachilungamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwaciwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda cifukwa.