Ezekiel 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unene kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Wadziitanira tsoka iwe mzinda umene umakhetsa magazi a anthu ake ambiri. Ndiwe mzinda umene umadziipitsa ndi mafano amene udadzipangira!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mudzi wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo unene kuti, ‘Ambuye akuti: Iwe mzinda umene wadzigwetsa wekha mʼtsoka pa kukhetsa magazi pakati pako ndi kudziyipitsa popanga mafano,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mudzi wokhetsa mwazi pakati pace, kuti nthawi yace ifike, nudzipangire mafano kudzidetsa nao.