Ezekiel 22:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidaŵakwiyira kwambiri. Ndidzaŵaononga kotheratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Motero ndidzaŵalanga monga kuŵayenera.” Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pa mutu pao, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndawakwiyira kwambiri. Ndawawonongeratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Ndawalanga molingana ndi zimene anachita. Akutero Ambuye Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yao yao ndinaibweza pa mutu pao, ati Ambuye Yehova.