Ezekiel 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wapalamula chifukwa cha kukhetsa magazi. Wadziipitsa chifukwa cha mafano amene udapanga. Motero wachepetsa masiku ako, ndipo zaka za moyo wako zatha. Nchifukwa chake ndalola kuti mitundu ya anthu ikunyoze, ndipo kuti maiko onse akuseke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wapalamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zakozako; chifukwa chake ndakuika ukhale chitonzo cha amitundu ndi choseketsa cha maiko onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
wapezekatu wolakwa chifukwa cha magazi amene wakhetsa, ndipo wadziyipitsa chifukwa cha mafano amene wapanga. Choncho wachepetsa masiku ako, ndipo zaka zako zafika kumapeto. Nʼchifukwa chake ndalola kuti anthu a mitundu ina akunyoze ndiponso kuti anthu a mayiko onse akuseke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.