Ezekiel 22:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa iwe muli ena ochita ugogodi kuti aphe anzao. Mulinso ena odyera zansembe pa zitunda zachipembedzo. Muli anthu enanso ochita zonyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa iwe muli anthu onenera anzawo zabodza kuti aphedwe. Mwa iwe mulinso amene amadyera zansembe pa mapiri a chipembedzo. Enanso amachita zonyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anacita zamanyazi.