Ezekiel 23:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adaamanga malamba m'chiwuno, ndi kuvala nduŵira kumutu. Onse ankaoneka ngati atsogoleri ankhondo, ndipo ankaoneka ngati Ababiloni, mbadwa za ku Kaldeya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
omangira malamba m'chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.