Ezekiel 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ankachitabe zadama zake osalekeza, namakumbukira zadama zimene ankachita pamene anali hule ku Ejipito pa ubwana wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anacurukitsa zigololo zace, nakumbukila masiku a ubwana wace, muja anacita cigololo m'dziko la Aigupto.