Ezekiel 23:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero iwe Oholiba udafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Ejipito ukadali namwali, kumene ankakusisita pa chifuwa, nkumakugwira maŵere ako osagwa aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo wautsanso choipa cha ubwana wako, pakukhudza Aejipito nsonga za mawere ako, chifukwa cha mawere a ubwana wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo wautsanso coipa ca ubwana wako, pakukhudza Aaigupto nsonga za maere ako, cifukwa ca maere a ubwana wako.