Ezekiel 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzabwera kuchokera kumpoto kudzakuthira nkhondo ndi akavalo ankhondo, magaleta ndi ngolo zambiri, ndiponso gulu lalikulu la ankhondo ochokera ku maiko onse. Adzakuzinga mbali zonse atavala malihawo, zishango ndi zisoti zankhondo. Ndidzakupereka m'manja mwao kuti akulange. Ndipo adzakulangadi monga momwe adzafunire iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakudzera ndi zida, magareta a nkhondo, ndi magareta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zocinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.