Ezekiel 23:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵalola kuti akuchite zankhanza chifukwa choti ndakukwiyira. Adzakudula mphuno ndi makutu, ndipo otsalira mwa iwe adzaŵapha ndi lupanga. Adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzapsa ndi moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakuchitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakuchotsera ana ako aamuna ndi aakazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakucitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakucotsera ana ako amuna ndi akazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.