Ezekiel 23:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Udzamwera chikho cha mkulu wako, chikho choloŵa ndiponso chachikulu. Anthu adzakuseka ndi kukunyoza, chifukwa chikhocho nchodzaza kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, M'chikho cha mkulu wako udzamweramo ndicho chachikulu ngati mchenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Udzamwera chikho cha mkulu wako, chikho chachikulu ndi chakuya; anthu adzakuseka ndi kukunyoza, pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, M'cikho ca mkuru wako udzamweramo ndico cacikuru ngati mcenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.