Ezekiel 23:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachita chigololo, ndipo adapha anthu. Adachita chigololo popembedza mafano ao, ndipo ana anga amene adandibalira, adaŵapereka kwa mafanowo ngati chakudya chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anacita cigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anacita cigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.