Ezekiel 23:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adangoti atapereka ana ao nsembe kwa mafano ao, nthaŵi yomweyo nkuloŵa m'Nyumba yanga yoyera naiipitsa. Ndithu zimenezi nzimene adachita m'Nyumba mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.