Ezekiel 23:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Komanso adatuma amithenga kukaitana amuna akutali. Anthuwo atabwera, abale aŵiri aja adasambasamba, nkukometsa m'masomu ndi utoto, navala zamakaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso munatuma kuitana anthu ochokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, chifukwa cha iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kuvala zokometsera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso munatuma kuitana anthu ocokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, cifukwa ca iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kubvala zokometsera;