Ezekiel 23:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Oholayo ankachita zadama ndi onsewo, amuna otchuka a ku Asiriya. Ndipo anakadziipitsa ndi mafano a amuna onse amene ankachita naye zadama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita nao zigololo zake, ndiwo anthu osankhika a ku Asiriya onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita nao zigololo zace, ndiwo anthu osankhika a ku Asuri onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.