Ezekiel 23:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadasiye makhalidwe ake a dama amene adaŵaphunzira ku Ejipito, kumene amuna ankagona naye akadali namwali. Ankamugwira maŵere akali anthete, namachita naye chigololo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye m'unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sanalekanso zigololo zace zocokera ku Aigupto, pakuti anagona naye m'unamwali wace, nakhudza maere a unamwali wace, namtsanulira cigololo cao.