Ezekiel 24:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, ndikulanda mwadzidzidzi mkazi wako amene amakukomera m'maso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikucotsera cokonda maso ako ndi cikomo, koma usamve cisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.