Ezekiel 24:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduŵira mudzavala ndithu ku mutu, nsapatonso mudzavala. Simudzalira maliro kapena kukhetsa misozi. Koma mudzavutika zedi chifukwa cha machimo anu, ndipo muzidzangodzumirana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu ku mapazi anu, simudzacita cisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzace.