Ezekiel 24:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsiku lina anthuŵa ndidzaŵachotsera linga lao limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkaŵakomera m'maso poliwona, limenenso ankaikapo mtima kwambiri. Ndidzaŵachotseranso ana ao aamuna ndi aakazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m'maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwacotsera mphamvu yao, cimwemwe cao copambana, cowakonda m'maso mwao, ndi cokhumbitsa mtima wao, ana ao amuna ndi akazi,